Lets write this one with bullet points.
-
Amwenye samangidwa unyolo akagwidwa, amalandira VIP treatment mpaka kumakwera galimoto ngati Minister, madzi akumwa ali m’manja.
-
Mabwana olima chamba obwera amangopatsidwa ma fine akagwidwa ndi chamba ndipo fine yake siyikhala ya serious kweni kweni, usually a suspended sentence and a maximum of 36 months.
-
Oweruza amatha kudzuka 12 koloko pakati pa usiku kukapereka bail ya Mabwana. Palibe anadzukako pakati pausiku kukapereka bail ya osawuka.
-
Mafana Ochepekedwa akalakwa timalandu topanda mayina amachita kunyongedwa ndi unyolo, m’galimoto amangoponyedwa kumbuyo uku Jombo ikuwachita kanthu. Akafika ku cell ambiri shape ya mitu yawo imakhala yasintha kumawoneka mwama corner chonchi.
-
Mafana Ochepekedwa mwayi wa bail supezeka kawili kawili. Mwayi wa lawyer sapatsidwa ndipo nthawi zina amakakamizidwa kuti angowuvomera mlanduwo.
-
Mafana Ochepekedwa amalandira chilango chowawa kwambiri poyerekeza ndi Mabwana amene amagwidwa ndi mlandu ngati omwewo. Ndende zadzadza ndi anthu opanda ma surname olozeka.
-
Nthawi idzakwana ndipo Ghetto idzayendetsa yokha milandu. Nthawi imeneyo mbamva tidzagwira tokha, milandu tidzazenga tokha ndipo chilango tidzaperekanso tokha.
Mphatso Dan Chitheka
Ndipo nkhani iyiyi imandiwawa…this is a very good example of Selective Justice. Mussah akuvutika cz ndi mfana ochepekedwa ngati ife
#JusticeForMussa
Bernard PM Kawonga
There’s selective justice in our country, principles of Justice are not being followed.
We need justice for Mussa John
Pride Msuku
Ndipo ndinkhani yokhayi osauka akanamvako pang’ono pokha kma
Augustine Mengwa
Mwana uja kukhala ndi ntaji wakatunde yeseyu kwawo sikukanala kovutika chonchija
Gerald Nthavi
Selective justice ndiyomwe ikutipweteka ðŸ˜ðŸ˜ðŸ˜